["Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana amuna, chitapita chigumula chija.","Ana amuna a Yafeti: Gomeri, ndi Magogi, ndi Madai, ndi Yavani, ndi Tubala, ndi Meseki ndi Tirasi.","Ndi ana amuna a Gomeri: Asikenazi, ndi Rifati, ndi Togarima.","Ndi ana amuna a Yavani: Elisa, ndi Tarisisi, ndi Kitimu, ndi Dodanimu.","Amenewo ndipo anagawa zisi za amitundu m'maiko mwao, onse amene monga mwa chinenedwe chao; ndi mwa mabanja ao, ndi m'mitundu yao.","Ndi ana amuna a Hamu: Kusi, ndi Ejipito, ndi Puti, ndi Kanani.","Ndi ana amuna a Kusi: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Raama, ndi Sabiteka; ndi ana a Raama: Sheba ndi Dedani.","Ndipo Kusi anabala Nimirodi; ndipo iye anayamba kukhala wamphamvu pa dziko lapansi.","Iye ndiye mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova: chifukwa chake kunanenedwa, Monga Nimirodi mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova.","Ndipo kuyamba kwake kwa ufumu wake kunali Babiloni, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m'dziko la Sinara.","M'dziko momwemo iye anatuluka kunka ku Asiriya, namanga Ninive, ndi mudzi wa Rehoboti, ndi Kala,","ndi Reseni pakati pa Ninive ndi Kala: umenewo ndi mudzi waukulu.","Ejipito ndipo anabala Ludimu, ndi Anamimu, ndi Lehabu, ndi Nafituhimu,","ndi Patirusimu, ndi Kasiluhimu, m'menemo ndipo anatuluka Afilisti, ndi Kafitori.","Ndipo Kanani anabala Sidoni woyamba wake, ndi Heti:","ndi Ayebusi, ndi Aamori, ndi Agirigasi;","ndi Ahivi, ndi Aariki, ndi Asini;","ndi Aaravadi, ndi Aazemari, ndi Ahamati; pambuyo pake pamenepo ndipo mabanja a Akanani anafalikira.","Ndipo malire a Akanani anayamba pa Sidoni, pakunka ku Gerari ndi ku Gaza; pakunka ku Sodomu, ndi ku Gomora, ndi Adima, ndi Zeboimu, kufikira ku Lasa.","Amenewa ndi ana amuna a Hamu monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.","Ndiponso kwa Semu atate wa ana onse a Eberi, mkulu wa Yafeti, kwa iye kunabadwa ana.","Ana amuna a Semu; Elamu, ndi Asiriya, ndi Aripakisadi, ndi Ludi, ndi Aramu.","Ndi ana a Aramu: Uzi ndi Huli ndi Getere, ndi Masi.","Aripakisadi ndipo anabala Sela; ndipo Sela anabala Eberi.","Kwa Eberi ndipo kunabadwa ana amuna awiri; dzina la wina ndi Pelegi; chifukwa kuti m'masiku ake dziko lapansi linagawanikana; dzina la mphwake ndi Yokotani.","Ndipo Yokotani anabala Alimodadi, ndi Selefi, ndi Hazara-Maveti, ndi Yera;","ndi Hadoramu ndi Uzali, ndi Dikila;","ndi Obala, ndi Abimaele, ndi Sheba;","ndi Ofiri ndi Havila, ndi Yobabu; onse amenewa ndi ana a Yokotani.","Kwao kunayamba pa Mesa pakunka ku Sefari phiri la kum'mawa.","Amenewa ndi ana a Semu, monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.","Amenewo ndi mabanja a ana a Nowa monga mwa mibadwo yao, m'mitundu yao: ndi amenewo anagawanika mitundu pa dziko lapansi, chitapita chigumula."]