["Ili ndi buku la mibadwo ya Adamu. Tsiku lomwe Mulungu analenga munthu anamlenga m'chifanizo cha Mulungu;","anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nawadalitsa iwo natcha mtundu wao anthu, tsiku lomwe anawalenga iwo.","Ndipo Adamu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza makumi atatu, nabala mwana wamwamuna m'chifanizo chake; namutcha dzina lake Seti.","Masiku ake Adamu atabala Seti, anali zaka mazana asanu ndi atatu; ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi.","Masiku ake onse anakhala ndi moyo Adamu anali zaka mazana asanu ndi anai, kudza makumi atatu; ndipo anamwalira.","Ndipo Seti anakhala ndi moyo zaka zana kudza zisanu, nabala Enosi;","ndipo Seti anakhala ndi moyo, atabala Enosi, zaka mazana asanu ndi atatu kudza zisanu ndi ziwiri: ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi:","masiku ake onse a Seti anali zaka mazana asanu ndi anai kudza khumi ndi ziwiri; ndipo anamwalira.","Ndipo Enosi anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi anai, nabala Kenani;","ndipo anakhala ndi moyo Enosi, atabala Kenani, zaka mazana asanu ndi atatu kudza khumi ndi zisanu: ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi.","Masiku ake onse a Enosi anali mazana asanu ndi anai kudza zisanu; ndipo anamwalira.","Ndipo Kenani anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi awiri, ndipo anabala Mahalalele:","ndipo Kenani anakhala ndi moyo, atabala Mahalalele zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi anai, ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi;","masiku ake onse a Kenani anali zaka mazana asanu ndi anai kudza khumi; ndipo anamwalira.","Ndipo Mahalalele anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu, nabala Yaredi;","ndipo Mahalalele anakhala ndi moyo, atabala Yaredi, zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi atatu, nabala ana aamuna ndi aakazi:","masiku ake onse a Mahalalele anali zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi asanu ndi anai ndi zisanu; ndipo anamwalira.","Ndipo Yaredi anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi limodzi ndi ziwiri, nabala Enoki;","ndipo Yaredi anakhala ndi moyo, atabala Enoki, zaka mazana asanu ndi atatu, nabala ana aamuna ndi aakazi;","masiku ake onse a Yaredi anali zaka mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu ndi limodzi ndi ziwiri: ndipo anamwalira.","Ndipo Enoki anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu, nabala Metusela:","ndipo Enoki anayendabe ndi Mulungu, atabala Metusela, zaka mazana atatu, nabala ana aamuna ndi aakazi;","masiku ake onse a Enoki anali mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi ndi zisanu;","ndipo Enoki anayendabe ndi Mulungu; ndipo panalibe iye; pakuti Mulungu anamtenga.","Ndipo Metusela anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi atatu ndi zisanu ndi ziwiri, nabala Lameki;","ndipo Metusela anakhala ndi moyo, atabala Lameki, zaka mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi atatu ndi awiri, nabala ana aamuna ndi aakazi:","masiku ake onse a Metusela anali mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi zinai; ndipo anamwalira.","Ndipo Lameki anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi atatu ndi ziwiri, nabala mwana wamwamuna;","namutcha dzina lake Nowa, ndi kuti, Yemweyu adzatonthoza mtima wathu pa ntchito zathu zovuta za manja athu, chifukwa cha nthaka imene anaitemberera Yehova;","ndipo Lameki anakhala ndi moyo atabala Nowa, zaka mazana asanu kudza makumi asanu ndi anai ndi zisanu, nabala ana aamuna ndi aakazi:","masiku ake onse a Lameki anali zaka mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi awiri; ndipo anamwalira.","Ndipo Nowa anali wa zaka mazana asanu; ndipo Nowa anabala Semu ndi Hamu ndi Yafeti."]