["Ndipo Yehosafati mfumu ya Yuda anabwerera kunyumba yake ku Yerusalemu mumtendere.","Natuluka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza zoipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova.","Koma zapezeka zokoma mwa inu, popeza mwazichotsa zifanizo m'dzikomo, mwalunjikitsanso mtima wanu kufuna Mulungu.","Ndipo Yehosafati anakhala ku Yerusalemu, natulukiranso mwa anthu kuyambira ku Beereseba kufikira ku mapiri a Efuremu; nawabweza atsatenso Yehova Mulungu wa makolo ao.","Naika oweruza m'dziko, m'midzi yonse yamalinga ya m'Yuda, mudzi ndi mudzi;","nati kwa oweruza, Khalani maso umo muchitira; pakuti simuweruzira anthu koma Yehova; ndipo ali nanu Iyeyu pakuweruza mlandu.","Ndipo tsono, kuopa Yehova kukhale pa inu, musamalire ndi kuchita; pakuti palibe chosalungama kwa Yehova Mulungu wathu, kapena kusamalira monga mwa nkhope ya munthu, kapena kulandira mphatso.","Yehosafati anaikanso m'Yerusalemu Alevi, ndi ansembe ena, ndi akulu a nyumba za makolo m'Israele, aweruzire Yehova, nanena milandu. Ndipo anabwerera kudza ku Yerusalemu.","Ndipo anawalangiza, ndi kuti, Muzitero ndi kuopa Yehova mokhulupirika ndi mtima wangwiro.","Ndipo ukakudzerani mlandu uliwonse wochokera kwa abale anu okhala m'midzi mwao, kusiyanitsa pakati pa mwazi ndi mwazi, pakati pa chilamulo ndi chiuzo, malemba ndi maweruzo, muwachenjeze kuti asapalamule kwa Yehova, angafikitsire inu nokha ndi abale anu mkwiyo; muzitero, ndipo simudzapalamula.","Ndipo taonani, Amariya wansembe wamkulu, ndiye mkulu wanu m'milandu yonse ya Yehova; ndi Zebadiya mwana wa Ismaele, wolamulira nyumba ya Yuda, m'milandu yonse ya mfumu; ndi Alevi akhale akapitao pamaso panu. Chitani molimbika mtima, ndipo Yehova akhale ndi abwino."]