["Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha, nati,","Kulamulira ndi kuopsa kuli ndi Iye;achita mtendere pa zam'mwamba zake.","Ngati awerengedwa makamu ake?Ndipo ndaniyo, kuunika kwake sikumtulukira?","Potero munthu akhala bwanji wolungama kwa Mulungu?Kapena wobadwa ndi mkazi akhala woyera bwanji?","Taonani, ngakhale mwezi ulibe kuwala;ndi nyenyezi siziyera pamaso pake;","kopambana kotani nanga munthu, ndiye mphutsi!Ndi wobadwa ndi munthu, ndiye nyongolotsi!"]