["Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati,","Munthu akayesa kunena nawe mau,kodi udzamva nao chisoni?Koma akhoza ndani kudziletsa kunena?","Taona iwe walangiza aunyinji,walimbitsa manja a ofooka.","Mau ako anachirikiza iye amene akadagwa,walimbitsanso maondo otewa.","Koma tsopano chakufikira iwe, ndipo ukomoka;chikukhudza, ndipo uvutika.","Kodi kulimbika mtima kwako si ndiko kuti uopa Mulungu,ndi chiyembekezo chako si ndiwo ungwiro wa njira zako?","Takumbukira tsopano, watayika ndani wosapalamula konse?Kapena oongoka mtima alikhidwa kuti?","Monga umo, ndaonera, olimira mphulupulu,nabzala vuto, akololapo zomwezo.","Atayika ndi mpweya wa Mulungu,nathedwa ndi mpumo wa mkwiyo wake.","Kubangula kwa mkango,ndi kulira kwa mkango waukali kwaletsedwa,ndi mano a misona ya mkango athyoledwa.","Mkango wokalamba udzifera posowa mkoka,ndi misona ya mkango waukazi imwazika.","Anditengera mau m'tseri,m'khutu mwanga ndinalandira kunong'oneza kwake.","M'malingaliro a masomphenya a usiku,powagwira anthu tulo tatikulu","Anandidzera mantha ndi kunjenjemera,nanthunthumira nako mafupa anga onse.","Pamenepo panapita mzimu pamaso panga;tsitsi la thupi langa lidati nyaunyau.","Unaima chilili, koma sindinatha kuzindikira maonekedwe ake;panali mzukwa pamaso panga;kunali chete, ndipo ndidamva mau akuti,","Kodi munthu adzakhala wolungama ndi kuposa Mulungu?Kodi munthu adzakhala woyera woposa Mlengi wake?","Taona, sakhulupirira atumiki ake;nawanenera amithenga ake zopusa;","kopambana kotani nanga iwo akukhala m'nyumba zadothi,amene kuzika kwao kuli m'fumbi,angothudzulidwa ngati njenjete.","Kuyambira m'mawa kufikira madzulo athudzuka;aonongeka kosatha, osasamalirako munthu.","Kukometsetsa kwao sikumachotsedwa nao?Amafa koma opanda nzeru."]