["Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi.","Tumikirani Yehova ndi chikondwerero:Idzani pamaso pake ndi kumuimbira mokondwera.","Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu;Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake;ndife anthu ake ndi nkhosa zapabusa pake.","Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko,ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo:Myamikeni; lilemekezeni dzina lake.","Pakuti Yehova ndiye wabwino;chifundo chake chimanka muyaya;ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo."]