["Ndidzaimba zachifundo ndi chiweruzo;ndidzaimba zakukulemekezani Inu, Yehova.","Ndidzachita mwanzeru m'njira yangwiro;mudzandidzera liti?Ndidzayenda m'nyumba mwanu ndi mtima wangwiro.","Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga;chochita iwo akupatuka padera chindiipira;sichidzandimamatira.","Mtima wopulukira udzandichokera;sindidzadziwana naye woipa.","Wakuneneza mnzake m'tseri ndidzamdula;wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.","Maso anga ayang'ana okhulupirika m'dziko, kuti akhale ndi Ine;iye amene ayenda m'njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine.","Wakuchita chinyengo sadzakhala m'kati mwa nyumba yanga;wakunena mabodza sadzakhazikika pamaso panga.","Mamawa onse ndidzadula oipa onse a m'dziko;kuduliratu onse akuchita zopanda pake kumudzi wa Yehova."]