["Wakhazikika mtima wanga, Mulungu;ndidzaimba, inde ndidzaimba zolemekeza, ndiko ulemerero wanga.","Galamukani, chisakasa ndi zeze;ndidzauka ndekha mamawa.","Ndidzakuyamikani mwa mitundu ya anthu, Yehova:ndipo ndidzaimba zakukulemekezani mwa anthu.","Pakuti chifundo chanu nchachikulu kupitirira kumwamba,ndi choonadi chanu kufikira mitambo.","Kwezekani pamwamba pa thambo, Mulungu;ndi ulemerero wanu pamwamba pa dziko lonse lapansi,","kuti okondedwa anu alanditsidwe,pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja ndipo mutivomereze.","Mulungu analankhula m'chiyero chake; ndidzakondwerera:ndidzagawa Sekemu; ndidzayesa muyeso chigwa cha Sukoti.","Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanga;ndi Efuremu ndiye mphamvu ya mutu wanga;Yuda ndiye wolamulira wanga.","Mowabu ndiye mkhate wanga;pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga;ndidzafuulira Filistiya.","Adzandifikitsa ndani m'mudzi wa m'linga?Adzanditsogolera ndani ku Edomu?","Si ndinu Mulungu, amene mwatitayaosatuluka nao magulu athu?","Tithandizeni mumsauko;pakuti chipulumutso cha munthu ndi chabe.","Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima:Ndipo Iye adzapondereza otisautsa."]