["Aleluya.Wodala munthu wakuopa Yehova,wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake.","Mbeu yake idzakhala yamphamvu pa dziko lapansi;mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa.","M'nyumba mwake mudzakhala akatundu ndi chuma:Ndi chilungamo chake chikhala chikhalire.","Kuunika kutulukira oongoka mtima mumdima;Iye ndiye wachisomo, ndi wansoni ndi wolungama.","Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa;adzalimbika nao mlandu wake poweruzidwa.","Popeza sadzagwedezeka nthawi zonse;wolungama adzakumbukika ku nthawi yosatha.","Sadzaopa mbiri yoipa;mtima wake ngwokhazika, wokhulupirira Yehova.","Mtima wake ngwochirikizika, sadzachita mantha,kufikira ataona chofuna iye pa iwo omsautsa.","Anagawagawa, anapatsa aumphawi;chilungamo chake chikhalitsa kosatha;nyanga yake idzakwezeka ndi ulemu.","Woipa adzaziona, nadzapsa mtima;adzakukuta mano, nadzasungunuka;chokhumba oipa chidzatayika."]