["Pulumutsani, Yehova; pakuti wofatsa wasowa;pakuti okhulupirika achepa mwa ana a anthu.","Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wake,amanena ndi mlomo wothyasika, ndi mitima iwiri.","Yehova adzadula milomo yonse yothyasika,lilime lakudzitamandira;","amene amati, Ndi lilime lathu tidzaposa;milomo yathu nja ife eni; mbuye wa pa ife ndani?","Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika,chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi,ndiuka tsopano, ati Yehova;ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo.","Mau a Yehova ndi mau oona;ngati siliva woyenga m'ng'anjo yadothi,yoiyeretsa kasanu ndi kawiri.","Mudzawasunga, Yehova,mudzawatchinjirizira mbadwo uno kunthawi zonse.","Oipa amayenda mozungulirazungulira,potamanda iwo chonyansa mwa ana a anthu."]