["Ndikweza maso anga kumapiri:Thandizo langa lidzera kuti?","Thandizo langa lidzera kwa Yehova,wakulenga zakumwamba ndi dziko lapansi.","Sadzalola phazi lako literereke:Iye amene akusunga sadzaodzera.","Taonani, wakusunga Israelesadzaodzera kapena kugona.","Yehova ndiye wakukusunga;Yehova ndiye mthunzi wako wa kudzanja lako lamanja.","Dzuwa silidzawamba usana,mwezi sudzakupanda usiku.","Yehova adzakusunga kukuchotsera zoipa zilizonse;adzasunga moyo wako.","Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako,kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse."]