["Ndinakondwera m'mene ananena nane,Tiyeni kunyumba ya Yehova.","Mapazi athu alinkuimam'zipata zanu, Yerusalemu","Yerusalemu anamangidwangati mudzi woundana bwino:","Kumene akwerako mafuko, ndiwo mafuko a Yehova;akhale mboni ya kwa Israele, Ayamike dzina la Yehova.","Pakuti pamenepo anaika mipando ya chiweruzo,mipando ya nyumba ya Davide.","Mupempherere mtendere wa Yerusalemu;akukonda inu adzaona phindu.","M'linga mwako mukhale mtendere,m'nyumba za mafumu mukhale phindu.","Chifukwa cha abale anga ndi mabwenzi anga,ndidzanena tsopano, Mukhale mtendere mwa inu.","Chifukwa cha nyumba ya Yehova Mulungu wathundidzakufunira zokoma."]