["Ndikweza maso anga kwa Inu,kwa Inu wakukhala kumwamba.","Taonani, monga maso a anyamataayang'anira dzanja la mbuye wao,monga maso a adzakaziayang'anira dzanja la mbuye wao wamkazi:Momwemo maso athu ayang'anira Yehova Mulungu wathu,kufikira atichitira chifundo.","Mutichitire chifundo, Yehova, mutichitire chifundo;pakuti takhuta kwambiri ndi mnyozo.","Moyo wathu wakhuta ndithundi kuseka kwa iwo osasowa kanthu,ndi mnyozo wa odzikuza."]