["Akadapanda kukhala nafe Yehova,anene tsono Israele;","Akadapanda kukhala nafe Yehova,pakutiukira anthu:","Akadatimeza amoyo,potipsera mtima wao.","Akadatimiza madziwo,mtsinje ukadapita pa moyo wathu;","madzi odzikuza akadapita pa moyo wathu.","Alemekezedwe Yehova,amene sanatipereke kumano kwao tikhale chakudya chao.","Moyo wathu unaonjoka ngati mbalame mu msampha wa msodzi;msampha unathyoka ndi ife tinaonjoka.","Thandizo lathu lili m'dzina la Yehova,wolenga kumwamba ndi dziko lapansi."]