["Iwo akukhulupirira Yehovaakunga phiri la Ziyoni, losasunthika, likhazikika kosatha.","Monga mapiri azinga Yerusalemu,momwemo Yehova azinga anthu ake,kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.","Pakuti ndodo yachifumu ya choipa siidzapumula pa gawo la olungama;kuti olungama asatulutse dzanja lao kuchita chosalungama.","Chitirani chokoma, Yehova, iwo okhala okoma;iwo okhala oongoka mumtima mwao.","Koma iwo akupatula kutsata njira zao zokhotakhota,Yehova adzawachotsa pamodzi ndi ochita zopanda pake.Mtendere ukhale pa Israele."]