["Akapanda kumanga nyumba Yehova,akuimanga agwiritsa ntchito chabe;akapanda kusunga mudzi Yehova,mlonda adikira chabe.","Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo,kudya mkate wosautsa kuupeza;kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m'tulo.","Taonani, ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova;chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake.","Ana a ubwana wake wa munthuakunga mivi m'dzanja lake la chiphona.","Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake:sadzachita manyazi iwo,pakulankhula nao adani kuchipata."]