["Wodala yense wakuopa Yehova,wakuyenda m'njira zake.","Pakuti udzadya za ntchito ya manja ako;wodala iwe, ndipo kudzakukomera.","Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m'mbali za nyumba yako;ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako.","Taonani, m'mwemo adzadalitsikamunthu wakuopa Yehova.","Yehova adzakudalitsa ali m'Ziyoni;ndipo udzaona zokoma za Yerusalemu masiku onse a moyo wako.","Inde, udzaona zidzukulu zako.Mtendere ukhala ndi Israele."]