["Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithukuti abale akhale pamodzi!","Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu,akutsikira kundevu,inde kundevu za Aroni;akutsikira kumkawo wa zovala zake.","Ngati mame a ku Heremoni,akutsikira pa mapiri a Ziyoni.Pakuti pamenepo Yehova analamulira dalitsolo,ndilo moyo womka muyaya."]