["Yamikani Yehova pakuti ndiye wabwino;pakuti chifundo chake nchosatha.","Yamikani Mulungu wa milungu;pakuti chifundo chake nchosatha.","Yamikani Mbuye wa ambuye;pakuti chifundo chake nchosatha.","Amene yekha achita zodabwitsa zazikulu;pakuti chifundo chake nchosatha.","Amene analenga zakumwamba mwanzeru;pakuti chifundo chake nchosatha.","Amene anayala dziko lapansi pamwamba pa madzi;pakuti chifundo chake nchosatha.","Amene analenga miuni yaikulu;pakuti chifundo chake nchosatha.","Dzuwa liweruze usana;pakuti chifundo chake nchosatha.","Mwezi ndi nyenyezi ziweruze usiku;pakuti chifundo chake nchosatha.","Iye amene anapandira Aejipito ana ao oyamba;pakuti chifundo chake nchosatha.","Natulutsa Israele pakati pao;pakuti chifundo chake nchosatha.","Ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka;pakuti chifundo chake nchosatha.","Amene anagawa magawo Nyanja Yofiira;pakuti chifundo chake nchosatha.","Napititsa Israele pakati pake;pakuti chifundo chake nchosatha.","Nakhuthula Farao ndi khamu lake m'Nyanja Yofiira:pakuti chifundo chake nchosatha.","Amene anatsogolera anthu ake m'chipululu;pakuti chifundo chake nchosatha.","Amene anapanda mafumu akulu;pakuti chifundo chake nchosatha.","Ndipo anawapha mafumu omveka;pakuti chifundo chake nchosatha.","Sihoni mfumu ya Aamori;pakuti chifundo chake nchosatha.","Ndi Ogi mfumu ya Basani;pakuti chifundo chake nchosatha.","Ndipo anapereka dziko lao likhale chosiyira;pakuti chifundo chake nchosatha.","Chosiyira cha kwa Israele mtumiki wake;pakuti chifundo chake nchosatha.","Amene anatikumbukira popepuka ife;pakuti chifundo chake nchosatha.","Natikwatula kwa otisautsa;pakuti chifundo chake nchosatha.","Ndiye wakupatsa nyama zonse chakudya;pakuti chifundo chake nchosatha.","Yamikani Mulungu wa kumwamba;pakuti chifundo chake nchosatha."]