["Aleluya,Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano,ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake.","Akondwere Israele mwa Iye amene anamlenga;ana a Ziyoni asekere mwa mfumu yao.","Alemekeze dzina lake ndi kuthira mang'ombe;amuimbire zomlemekeza ndi lingaka ndi zeze.","Popeza Yehova akondwera nao anthu ake;adzakometsa ofatsa ndi chipulumutso.","Okondedwa ake atumphe mokondwera m'ulemu:Afuule mokondwera pamakama pao.","Nyimbo zakukweza Mulungu zikhale pakamwa pao,ndi lupanga lakuthwa konsekonse m'dzanja lao;","kubwezera chilango akunja,ndi kulanga mitundu ya anthu;","kumanga mafumu ao ndi maunyolo,ndi omveka ao ndi majerejede achitsulo,","kuwachitira chiweruzo cholembedwacho.Ulemu wa okondedwa ake onse ndi uwu.Aleluya."]