["Yehova akuvomereze tsiku la nsautso;dzina la Mulungu wa Yakobo likuike pamsanje;","likutumizire thandizo lotuluka m'malo oyera,ndipo likugwirizize kuchokera m'Ziyoni;","likumbukire zopereka zako zonse,lilandire nsembe yako yopsereza;","likupatse cha mtima wako,ndipo likwaniritse upo wako wonse.","Tidzafuula mokondwera mwa chipulumutso chanu,ndipo m'dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera;Yehova akwaniritse mapempho ako onse.","Tsopano ndidziwa kuti Yehova apulumutsa wodzozedwa wake;adzamvomereza m'Mwamba mwake moyerandi mphamvu ya chipulumutso cha dzanja lake lamanja.","Ena atama magaleta, ndi ena akavalo;koma ife tidzatchula dzina la Yehova Mulungu wathu.","Iwowa anagonjeka, nagwa;koma ife tauka, ndipo takhala chilili.","Yehova, pulumutsani,mfumuyo ativomereze tsiku lakuitana ife."]