["Mundiweruze, Yehova, pakuti ndayenda m'ungwiro wanga,ndipo ndakhulupirira Yehova, sindadzaterereka.","Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe;yeretsani impso zanga ndi mtima wanga.","Pakuti chifundo chanu chili pamaso panga;ndipo ndayenda m'choona chanu.","Sindinakhala pansi ndi anthu achabe;kapena kutsagana nao anthu othyasika.","Ndidana nao msonkhano wa ochimwa,ndipo sindidzakhala nao pansi ochita zoipa.","Ndidzasamba manja anga mosalakwa;kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova;","kuti ndimveketse mau a chiyamiko,ndi kulalikira ntchito zanu zonse zozizwa.","Yehova, ndikonda chikhalidwe cha nyumba yanu,ndi malo akukhalamo ulemerero wanu.","Musandichotsere mzimu wanga pamodzi ndi olakwa,kapena moyo wanga pamodzi ndi anthu okhetsa mwazi;","amene m'manja mwao muli mphulupulu,ndi dzanja lao lamanja ladzala ndi zokometsera mlandu.","Koma ine, ndidzayenda m'ungwiro wanga;mundiombole, ndipo ndichitireni chifundo.","Phazi langa liponda pachidikha,m'masonkhano ndidzalemekeza Yehova."]