["Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira;thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva;pakuti ngati munditontholera ine,ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.","Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu,pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera.","Musandikoke kundichotsa pamodzi ndi oipa,ndi ochita zopanda pake;amene alankhula zamtendere ndi anansi ao,koma mumtima mwao muli choipa.","Muwapatse monga mwa ntchito zao,ndi monga mwa choipa chochita iwo;muwapatse monga mwa machitidwe a manja ao;muwabwezere zoyenera iwo.","Pakuti sasamala ntchito za Yehova,kapena machitidwe a manja ake,adzawapasula, osawamanganso.","Wodalitsika Yehova, Pakuti adamva mau a kupemba kwanga.","Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa;mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza,chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu;ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.","Yehova ndiye mphamvu yao,inde mphamvu ya chipulumutso cha wodzozedwa wake.","Pulumutsani anthu anu, ndi kudalitsa cholandira chanu;muwawetenso, ndi kuwanyamula nthawi zonse."]