["Perekani kwa Yehova, inu ana a amphamvu,perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.","Perekani kwa Yehova ulemerero wa dzina lake,gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa.","Liu la Yehova lili pamadzi;Mulungu wa ulemerero agunda,ndiye Yehova pa madzi ambiri.","Liu la Yehova ndi lamphamvu;liu la Yehova ndi lalikulukulu.","Liu la Yehova lithyola mitengo yamkungudza;inde Yehova athyola mikungudza ya ku Lebanoni.","Aitumphitsa monga mwanawang'ombe;Lebanoni ndi Sirioni monga msona wa njati.","Liu la Yehova ligawa malawi a moto.","Liu la Yehova ligwedeza chipululu;Yehova agwedeza chipululu cha Kadesi.","Liu la Yehova liswetsa nyama zazikazi,ndipo lipulula nkhalango;ndipo m'Kachisi mwake zonse zili m'mwemo zimati, Ulemerero.","Yehova anakhala pa chigumula,inde Yehova akhala mfumu kunthawi yonka muyaya.","Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu,Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendere."]