["Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa;pondichepera mwandikulitsira malo.Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.","Amuna inu, ulemu wanga udzakhala wamanyazi kufikira liti?Mudzakonda zachabe, ndi kufunafuna bodza kufikira liti?","Koma dziwani kuti Yehova anadzipatulira yekha womkondayo,adzamva Yehova m'mene ndimfuulira Iye.","Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe.Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete.","Iphani nsembe za chilungamo,ndipo mumkhulupirire Yehova.","Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani?Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.","Mwapatsa chimwemwe mumtima mwanga,chakuposa chao m'nyengo yakuchuluka dzinthu zao ndi vinyo wao.","Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo;chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino."]