["Kuyembekeza ndayembekeza Yehova;ndipo anandilola, namva kufuula kwanga.","Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko,ndi m'thope la pachithaphwi;nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.","Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga,chilemekezo cha kwa Mulungu wanga;ambiri adzachiona, nadzaopa,ndipo adzakhulupirira Yehova.","Wodala munthuyo wakuyesa Yehova wokhulupirika;wosasamala odzikuza, ndi opatukira kubodza.","Inu, Yehova, Mulungu wanga,zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri,ndipo zolingirira zanu za pa ife;palibe wina wozifotokozera Inu;ndikazisimba ndi kuzitchula,zindichulukira kuziwerenga.","Nsembe ndi chopereka simukondwera nazo;mwanditsegula makutu.Nsembe yopsereza ndi yamachimo simunapempha.","Pamenepo ndinati, Taonani, ndadza;m'buku mwalembedwa za Ine,","kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga;ndipo malamulo anu ali m'kati mwamtima mwanga.","Ndalalikira chilungamo mu msonkhano waukulu;onani, sindidzaletsa milomo yanga,mudziwa ndinu Yehova.","Chilungamo chanu sindinachibisa m'kati mwamtima mwanga;chikhulupiriko chanu ndi chipulumutso chanu ndinachinena;chifundo chanu ndi choonadi chanusindinachibisira msonkhano waukulu.","Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu,chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire.","Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga,zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya;ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima.","Ndikupemphani, Yehova, ndilanditseni;fulumirani kudzandithandiza, Yehova.","Achite manyazi nadodomeiwo akulondola moyo wanga kuti auononge.Abwerere m'mbuyo, nachite manyaziiwo okondwera kundichitira choipa.","Apululuke, mobwezera manyazi aoamene anena nane, Hede, hede.","Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu;iwo akukonda chipulumutso chanuasaleke kunena, Abuke Yehova.","Ndipo ine ndine wozunzika ndi waumphawi;koma Ambuye andikumbukira ine.Inu ndinu mthandizi wanga, ndi Mpulumutsi wanga,musamachedwa, Mulungu wanga."]