["Ombani m'manja, mitundu yonse ya anthu;fuulirani kwa Mulungu ndi liu la kuimbitsa.","Pakuti Yehova Wam'mwambamwamba ndiye woopsa;ndiye mfumu yaikulu pa dziko lonse lapansi.","Atigonjetsera anthu,naika amitundu pansi pa mapazi athu.","Atisankhira cholowa chathu,chokometsetsa cha Yakobo amene anamkonda.","Mulungu wakwera ndi mfuu,Yehova ndi liu la lipenga.","Imbirani Mulungu, imbirani;imbirani mfumu yathu, imbirani.","Pakuti Mulungu ndiye mfumu ya dziko lonse lapansi;imbirani ndi chilangizo.","Mulungu ndiye mfumu ya amitundu,Mulungu akhala pa mpando wachifumu wake woyera.","Akulu a anthu asonkhanaakhale anthu a Mulungu wa Abrahamu,pakuti zikopa za dziko lapansi nza Mulungu;akwezeka kwakukulu Iyeyo."]