["Chitsiru chimati mumtima mwake, Kulibe Mulungu.Achita zovunda, achita chosalungama chonyansa;kulibe wakuchita bwino.","Mulungu m'mwamba anaweramira pa ana a anthu,kuti aone ngati aliko wanzeru,wakufuna Mulungu.","Onse anabwerera; anavunda mtima pamodzi;palibe mmodzi wakuchita bwino, nnena mmodzi.","Kodi ochita zopanda pake sadziwa?Pomadya anthu anga monga akudya mkate;ndipo saitana Mulungu.","Pamenepo anaopa kwakukulu, popanda chifukwa cha kuopa,pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe;unawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza.","Ha, chipulumutso cha Israele chichokere m'Ziyoni!Pakubweretsa Mulungu anthu ake a m'ndende,Yakobo adzakondwera, Israele adzasekera."]