["Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo;pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu,ndipo ndithawira kumthunzi wa mapiko anu,kufikira zosakazazo zidzapita.","Ndidzafuulira kwa Mulungu Wam'mwambamwamba;ndiye Mulungu wonditsirizira zonse.","Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsaponditonza wofuna kundimeza;Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake.","Moyo wanga uli pakati pa mikango;ndigona pakati pa oyaka moto,ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi,ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthawa.","Mukwezeke m'mwambamwamba, Mulungu;ulemerero wanu ukhale pamwamba pa dziko lonse lapansi.","Ananditchera ukonde apo ndiyenda;moyo wanga wawerama.Anandikumbira mbuna patsogolo panga;anagwa m'kati mwake iwo okha.","Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima;ndidzaimba, inde, ndidzaimba zolemekeza.","Galamuka, ulemu wanga; galamukani chisakasa ndi zeze!Ndidzauka ndekha mamawa.","Ndidzakuyamikirani mwa anthu, Ambuye,ndidzakuimbirani mwa mitundu.","Pakuti chifundo chanu nchachikulu kufikira m'mwamba,ndi choonadi chanu kufikira mitambo.","Kwezekani m'mwambamwamba, Mulungu;ulemerero wanu ukhale pamwamba m'dziko lonse lapansi."]