["Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu,ndipo musandilange m'kukali wanu.","Mundichitire chifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine.Mundichize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga.","Moyo wanganso wanthunthumira kwakukulu;ndipo Inu, Yehova, kufikira liti?","Bwererani Yehova, landitsani moyo wanga;ndipulumutseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu.","Pakuti muimfa m'mosakumbukira Inu;m'mandamo adzakuyamikani ndani?","Ndalema nako kuusa moyo kwanga;ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse;mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.","Lapuwala diso langa chifukwa cha chisoni;lakalamba chifukwa cha onse akundisautsa.","Chokani kwa ine, nonsenu akuchita zopanda pake;pakuti wamva Yehova mau a kulira kwanga.","Wamva Yehova kupemba kwanga;Yehova adzalandira pemphero langa.","Adzachita manyazi, nadzanthunthumira kwakukuluadani anga onse;adzabwerera, nadzachita manyazi modzidzimuka."]