["Mwatitaya Mulungu, mwatipasula;mwakwiya; tibwezereni.","Mwagwedeza dziko, mwaling'amba.Konzani ming'alu yake; pakuti ligwedezeka.","Mwaonetsa anthu anu zowawa,mwatimwetsa vinyo wotinjenjemeretsa.","Koma mwapatsa mbendera akuopa Inu,aikweze chifukwa cha choonadi.","Kuti okondedwa anu alanditsidwe,pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja, ndipo mutivomereze.","Mulungu walankhula m'chiyero chake; ndidzakondwerera,ndidzagawa Sekemu, ndidzayesa muyeso chigwa cha Sukoti.","Giliyadi ndi wanga, Manasenso ndi wanga;ndipo Efuremu ndi mphamvu ya mutu wanga;Yuda ndiye wolamulira wanga.","Mowabu ndiye mkhate wanga;pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga.Filistiya, fuulatu chifukwa cha ine.","Adzandifikitsa ndani m'mudzi wa m'linga?Adzanditsogolera ndani ku Edomu?","Si ndinu, Mulungu, amene mwatitaya?Osatuluka nao makamu athu, Mulungu.","Tithandizeni kunsautso;kuti chipulumutso cha munthu ndi chabe.","Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima,ndipo Iye adzapondereza otisautsa."]