["Imvani mfuu wanga, Mulungu;mverani pemphero langa.","Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu,pomizika mtima wanga.Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake.","Pakuti munakhala pothawirapo panga;nsanja yolimba pothawa mdani ine.","Ndidzagoneragonerabe m'chihema mwanu;ndidzathawira mobisalamo m'mapiko anu.","Pakuti Inu, Mulungu, mudamva zowinda zanga;munandipatsa cholowa cha iwo akuopa dzina lanu.","Mudzatalikitsa moyo wa mfumu.Zaka zake zidzafikira mibadwomibadwo.","Adzakhala nthawi zonse pamaso pa Mulungu;mumpatse chifundo ndi choonadi zimsunge.","Potero ndidzaimba zolemekeza dzina lanu kunthawi zonse,kuti ndichite zowinda zanga tsiku ndi tsiku."]