["Fuulirani kwa Mulungu, dziko lonse lapansi.","Imbirani ulemerero wa dzina lake;pomlemekeza mumchitire ulemerero.","Nenani kwa Mulungu, Ha,ntchito zanu nzoopsa nanga!Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu.","Dziko lonse lapansi lidzakugwadirani,ndipo lidzakuimbirani;ndzaimbira dzina lanu.","Idzani, muone ntchito za Mulungu;zochitira Iye ana a anthu nzoopsa.","Anasanduliza nyanja ikhale mtunda.Anaoloka mtsinje choponda pansi,apo tinakondwera mwa Iye.","Achita ufumu mwa mphamvu yake kosatha;maso ake ayang'anira amitundu;opikisana ndi Iye asadzikuze.","Lemekezani Mulungu wathu, mitundu ya anthu inu,ndipo mumveketse liu la chilemekezo chake.","Iye amene asunga moyo wathu tingafe,osalola phazi lathu literereke.","Pakuti munatiyesera, Mulungu,munatiyenga monga ayenga siliva.","Munapita nafe kuukonde;munatisenza chothodwetsa pamsana pathu.","Munapititsa anthu oberekeka pamwamba pamitu pathu;tinapyola moto ndi madzi;koma munatifikitsa potitsitsimutsa.","Ndidzalowa m'nyumba yanu ndi nsembe zopsereza,ndidzakuchitirani zowinda zanga,","zimene inazitchula milomo yanga,ndinazinena pakamwa panga posautsika ine.","Ndidzakufukizirani nsembe zopsereza zonona,pamodzi ndi chofukiza cha mphongo za nkhosa;ndidzakonza ng'ombe pamodzi ndi mbuzi.","Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu,ndipo ndidzafotokozera zonse anazichitira moyo wanga.","Ndinamfuulira Iye pakamwa panga,ndipo ndinamkuza ndi lilime langa.","Ndikadasekera zopanda pake m'mtima mwanga,Ambuye sakadamvera.","Koma Mulungu anamvadi;anamvera mau a pemphero langa.","Wolemekezeka Mulungu,amene sanandipatutsire ine pemphero langa,kapena chifundo chake."]