["Atichitire chifundo Mulungu, ndi kutidalitsa,atiwalitsire nkhope yake;","kuti njira yanu idziwike pa dziko lapansi,chipulumutso chanu mwa amitundu onse.","Anthu akuyamikeni, Mulungu;anthu onse akuyamikeni.","Anthu akondwere, nafuule mokondwera;pakuti mudzaweruza anthu molunjika,ndipo mudzalangiza anthu pa dziko lapansi.","Anthu akuyamikeni, Mulungu;anthu onse akuyamikeni.","Dziko lapansi lapereka zipatso zake,Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa.","Mulungu adzatidalitsa;ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzamuopa Iye."]