["Fulumirani kundipulumutsa, Mulungu!Fulumirani kundithandiza, Yehova.","Achite manyazi, nadodomeamene afuna moyo wanga.Abwezedwe m'mbuyo, napepulidweamene akonda kundichitira choipa.","Abwerere, kukhale mphotho ya manyazi aoamene akuti, Hede, hede.","Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu;nanene kosalekeza iwo akukonda chipulumutso chanu,abuke Mulungu.","Koma ine ndine wozunzika ndi waumphawi;mundifulumirire, Mulungu.Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga;musachedwe, Yehova."]