["Ndikhulupirira Inu, Yehova.Ndisachite manyazi nthawi zonse.","Ndikwatuleni m'chilungamo chanu, ndi kundilanditsa,nditcherereni khutu lanu ndi kundipulumutsa.","Mundikhalire thanthwe lokhalamo, lopitako kosaleka;mwalamulira kundipulumutsa;popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.","Ndilanditseni, Mulungu wanga, m'dzanja la woipa,m'dzanja la munthu wosalungama ndi wachiwawa.","Pakuti Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova;mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.","Inu munandigwiriziza kuyambira ndisanabadwe,kuyambira pa thupi la mai wanga wondichitira zokoma ndinu;ndidzakulemekezani kosalekeza.","Ndikhala chodabwitsa kwa ambiri;koma Inu ndinu pothawira panga polimba.","M'kamwa mwanga mudzadzala lemekezo lanu,ndi ulemu wanu tsiku lonse.","Musanditaye mu ukalamba wanga;musandisiye, pakutha mphamvu yanga.","Pakuti adani anga alankhula za ine;ndipo iwo akulalira moyo wanga apangana upo,","ndi kuti, Wamsiya Mulungu.Mlondoleni, mgwireni; popeza palibe wompulumutsa.","Musandikhalire kutali, Mulungu;fulumirani kundithandiza, Mulungu.","Adani a moyo wanga achite manyazi, nathawe;chotonza ndi chimpepulo zikute ondifunira choipa.","Koma ine ndidzayembekeza kosaleka,ndipo ndidzaonjeza kukulemekezani.","Pakamwa panga padzafotokozera chilungamo chanu,ndi chipulumutso chanu tsiku lonse;pakuti sindidziwa mawerengedwe ake.","Ndidzamuka mu mphamvu ya Ambuye Yehova;ndidzatchula chilungamo chanu, inde chanu chokha.","Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga;ndipo kufikira lero ndilalikira zodabwitsa zanu.","Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu;kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu,mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo.","Chilungamo chanunso, Mulungu, chifikira kuthambo;Inu amene munachita zachikulu,akunga Inu ndani, Mulungu?","Inu, amene munationetsa nsautso zambiri ndi zoipa,mudzatipatsanso moyo,ndi kutitenganso munsi mwa dziko.","Mundionjezere ukulu wanga,ndipo munditembenukire kundisangalatsa.","Ndiponso ndidzakuyamikani ndi chisakasa,kubukitsa choonadi chanu, Mulungu wanga;ndidzakuimbirani nyimbo ndi zeze,ndinu Woyerayo wa Israele.","Milomo yanga idzafuula mokondwera poimbira Inu nyimbo;inde, moyo wanga umene munaombola.","Lilime langa lomwe lidzalankhula za chilungamo chanu tsiku lonse,pakuti ofuna kundichitira choipa achita manyazi, nadodoma."]