["Mulungu adziwika mwa Yuda,dzina lake limveka mwa Israele.","Msasa wake unali m'Salemu,ndipo pokhala Iye m'Ziyoni.","Pomwepo anathyola mivi ya pauta;chikopa, ndi lupanga, ndi nkhondo.","Inu ndinu wakuunikira, ndi womvekawakuposa mapiri muli achifwamba.","Olimba mtima chifunkhidwa chuma chao, agona tulo tao;amuna onse amphamvu asowa manja ao.","Pa kudzudzula kwanu, Mulungu wa Yakobo,galeta ndi kavalo yemwe anagwa m'tulo.","Inu ndinu woopsa;ndipo utauka mkwiyo wanu adzakhala chilili ndani pamaso panu?","Mudamveketsa chiweruzo chochokera Kumwamba;dziko lapansi linachita mantha, nilinakhala chete,","pakuuka Mulungu kuti aweruze,kuti apulumutse ofatsa onse a pa dziko lapansi.","Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani;chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.","Windani ndipo chitirani Yehova Mulungu wanu zowindazo;onse akumzinga abwere nacho choperekacha kwa Iye amene ayenera kumuopa.","Iye adzadula mzimu wa akulu;akhala woopsa kwa mafumu a pa dziko lapansi."]