["Mulungu aima mu msonkhano wa Mulungu,aweruza pakati pa milungu.","Mudzaweruza mosalunjika kufikira liti,ndi kusamalira nkhope ya oipa?","Weruzani osauka ndi amasiye;weruzani molungama ozunzika ndi osowa.","Pulumutsani osauka ndi aumphawi;alanditseni m'dzanja la oipa.","Sadziwa, ndipo sazindikira;amayendayenda mumdima;maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.","Ndinati Ine, Inu ndinu milungu,ndi ana a Wam'mwambamwamba nonsenu.","Komatu mudzafa monga anthu,ndipo mudzagwa monga wina wa akulu.","Ukani, Mulungu, weruzani dziko lapansi;pakuti Inu mudzalandira amitundu onse."]