["Munachita zovomereza dziko lanu, Yehova;munabweza ukapolo wa Yakobo.","Munachotsa mphulupulu ya anthu anu,munafotsera zolakwa zao zonse.","Munabweza kuzaza kwanu konse;munabwerera kumkwiyo wanu wotentha.","Mutibweze, Mulungu wa chipulumutso chathu,nimuletse udani wanu wa pa ife.","Kodi mudzatikwiyira nthawi zonse?Kodi mudzakhala chikwiyire mibadwomibadwo?","Kodi simudzatipatsanso moyo,kuti anthu anu akondwerere ndi Inu?","Tionetseni chifundo chanu, Yehova,tipatseni chipulumutso chanu.","Ndidzamva cholankhula Mulungu Yehova;pakuti adzalankhula zamtendere ndi anthu ake,ndi okondedwa ake;koma asabwererenso kuchita zopusa.","Indedi chipulumutso chake chili pafupindi iwo akumuopa Iye;kuti m'dziko mwathu mukhale ulemu.","Chifundo ndi choonadi zakomanizana;chilungamo ndi mtendere zapsompsonana.","Choonadi chiphukira m'dziko;ndi chilungamo chasuzumira chili m'mwamba.","Inde Yehova adzapereka zokoma;ndipo dziko lathu lidzapereka zipatso zake.","Chilungamo chidzamtsogolera;nichidzamkonzera mapazi ake njira."]