["Nkokoma kuyamika Yehova,ndi kuimbira nyimbo dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu.","Kuonetsera chifundo chanu mamawa,ndi chikhulupiriko chanu usiku uliwonse.","Pa choimbira cha zingwe khumi ndi pachisakasa;pazeze ndi kulira kwake.","Popeza Inu, Yehova, munandikondweretsa ndi kuchita kwanu,ndidzafuula mokondwera pa ntchito ya manja anu.","Ha! Ntchito zanu nzazikulu, Yehova,zolingalira zanu nzozama ndithu.","Munthu wopulukira sachidziwa;ndi munthu wopusa sachizindikira ichi;","chakuti pophuka oipa ngati msipu,ndi popindula ochita zopanda pake;chitero kuti adzaonongeke kosatha.","Koma Inu, Yehova, muli m'mwamba kunthawi yonse.","Pakuti, taonani, adani anu, Yehova,pakuti, taonani, adani anu adzatayika;ochita zopanda pake onse adzamwazika.","Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati;anandidzoza mafuta atsopano.","Diso langa lapenya chokhumba ine pa iwo ondilalira,m'makutu mwanga ndamva chokhumba inepa iwo akuchita zoipa akundiukira.","Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa;adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni.","Iwo ookedwa m'nyumba ya Yehova,adzaphuka m'mabwalo a Mulungu wathu.","Atakalamba adzapatsanso zipatso;adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri,","kulalikira kuti Yehova ngwolunjika;Iye ndiye thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama."]