["Yehova achita ufumu; dziko lapansi likondwere;zisumbu zambiri zikondwerere.","Pomzinga pali mitambo ndi mdima;chilungamo ndi chiweruzo ndizo zolimbitsampando wachifumu wake.","Moto umtsogolera,nupsereza otsutsana naye pozungulirapo.","Mphezi zake zinaunikira dziko lokhalamo anthu;dziko lapansi linaona nilinagwedezeka.","Mapiri anasungunuka ngati sera pamaso pa Yehova,pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.","Kumwamba kulalikira chilungamo chake,ndipo mitundu yonse ya anthu ipenya ulemerero wake.","Onse akutumikira fano losema,akudzitamandira nao mafano, achite manyazi:Mgwadireni Iye, milungu yonse inu.","Ziyoni anamva nakondwera,nasekerera ana akazi a Yuda;chifukwa cha maweruzo anu, Yehova.","Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba pa dziko lonse lapansi,ndinu wokwezeka kwakukulu pamwamba pa milungu yonse ina.","Inu okonda Yehova, danani nacho choipa:Iye asunga moyo wa okondedwa ake;awalanditsa m'manja mwa oipa.","Kuunika kufesekera wolungama,ndi chikondwerero oongoka mtima.","Kondwerani mwa Yehova, olungama inu;ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake."]