["Ndipo maina a ana a Israele, amene analowa m'Ejipito ndi Yakobo ndi awa, analowa munthu ndi banja lake:","Rubeni, Simeoni, Levi ndi Yuda;","Isakara, Zebuloni, ndi Benjamini;","Dani ndi Nafutali, Gadi ndi Asere.","Ndipo amoyo onse amene anatuluka m'chuuno mwake mwa Yakobo ndiwo makumi asanu ndi awiri; koma Yosefe anali m'Ejipito.","Ndipo anafa Yosefe, ndi abale ake onse, ndi mbadwo uwo wonse.","Ana a Israele ndipo anaswana, nabalana, nachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu; ndipo dziko linadzala nao.","Pamenepo inalowa mfumu yatsopano m'ufumu wa Ejipito, imene siinadziwa Yosefe.","Ndipo ananena ndi anthu ake, Taonani, anthu, ndiwo ana a Israele, achuluka, natiposa mphamvu.","Tiyeni, tiwachenjerere angachuluke, ndi kuphatikizana ndi adani athu ikafika nkhondo, ndi kulimbana nafe, ndi kuchoka m'dzikomo.","Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao midzi yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi.","Koma monga momwe anawasautsiramo, momwemo anachuluka, momwemonso anafalikira. Ndipo anavutika chifukwa cha ana Israele.","Ndipo Aejipito anawagwiritsa ana a Israele ntchito yosautsa;","nawawitsa moyo wao ndi ntchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi ntchito zonse za pabwalo, ntchito zao zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa.","Ndipo mfumu ya Aejipito inanena ndi anamwino a Ahebri, dzina lake la wina ndiye Sifira, dzina la mnzake ndiye Puwa;","ninati, Pamene muchiza akazi a Ahebri nimuwaone pamipando; akakhala mwana wamwamuna, mumuphe; akakhala wamkazi, akhale ndi moyo.","Koma anamwino anaopa Mulungu, ndipo sanachite monga mfumu ya Aejipito inawauza, koma analeka ana amuna akhale ndi moyo.","Ndipo mfumu ya Aejipito inaitana anamwino, ninena nao, Mwachita ichi chifukwa ninji, ndi kuleka ana amunawo akhale ndi moyo?","Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aejipito; pakuti ali ndi mphamvu, naona ana asanafike anamwino.","Potero Mulungu anawachitira zabwino anamwino; ndipo anthuwo anachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu.","Ndipo kunatero kuti, popeza anamwino anaopa Mulungu, Iye anawamangitsira mabanja.","Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana amuna onse akabadwa aponyeni m'nyanja, koma ana akazi onse alekeni amoyo."]