["Pamenepo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao, numuuze, Atero Yehova Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire.","Pakuti ukakana kuwalola amuke, ndi kuwagwira chigwiritsire,","taona, dzanja la Yehova lidzakhala pa zoweta zako za kubusa, pa akavalo, pa abulu, pa ngamira, pa ng'ombe, ndi pa zoweta zazing'ono ndi kalira woopsa.","Ndipo Yehova adzasiyanitsa pakati pa zoweta za Israele ndi zoweta za Ejipito; kuti kasafe kanthu kalikonse ka ana a Israele.","Ndipo Yehova anaika nthawi yakuti, nati, Mawa Yehova adzachita chinthu ichi m'dzikomu.","Ndipo m'mawa mwake Yehova anachita chinthucho, ndipo zinafa zoweta zonse za m'Ejipito; koma sichinafa chimodzi chonse cha zoweta za ana a Israele.","Ndipo Farao anatuma, taonani, sichidafa chingakhale chimodzi chomwe cha zoweta za Aisraele. Koma mtima wa Farao unauma, ndipo sanalole anthu amuke.","Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Tengani phulusa la ng'anjo lodzala manja; ndi Mose aliwaze kuthambo pamaso pa Farao.","Ndipo lidzakhala fumbi losalala pa dziko lonse la Ejipito, ndipo lidzakhala pa anthu ndi pa zoweta ngati zilonda zobuka ndi matuza, m'dziko lonse la Ejipito.","Ndipo anatenga phulusa la m'ng'anjo, naima pamaso pa Farao; ndi Mose analiwaza kuthambo; ndipo linakhala zilonda zobuka ndi matuza pa anthu ndi pa zoweta.","Ndipo alembi sanakhoza kuima pamaso pa Mose chifukwa cha zilondazo; popeza panali zilonda pa alembi ndi pa Aejipito onse.","Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, kuti sanamvere iwo; monga Yehova adalankhula ndi Mose.","Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uka nulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao, nunene naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, akanditumikire.","Pakuti nthawi yino ndidzatuma miliri yanga yonse pamtima pako, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako; kuti udziwe kuti palibe wina wonga Ine pa dziko lonse lapansi.","Pakuti ndatambasula dzanja langa tsopano, kuti ndikupande iwe ndi anthu ako ndi mliri, ndi kuti uonongeke pa dziko lapansi.","Koma ndithu chifukwa chake ndakuimika kuti ndikuonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa pa dziko lonse lapansi.","Kodi udzikwezanso pa anthu anga, ndi kusawalola amuke?","Taona, mawa monga nthawi yino ndidzavumbitsa mvumbi wa matalala, sipadakhala unzake m'Ejipito kuyambira tsiku lija lidakhazikika kufikira lero lino.","Ndipo tsopano, tumiza, thawitsa zoweta zako ndi zonse uli nazo pabwalo; pakuti anthu onse ndi zoweta zonse zopezeka pabwalo, zosasonkhanidwa m'nyumba, matalala adzazigwera, ndipo zidzafa.","Iyeyu wa anyamata a Farao wakuopa mau a Yehova anathawitsira m'zinyumba anyamata ake ndi zoweta zake;","koma iyeyu wosasamalira mau a Yehova anasiya anyamata ndi zoweta zake kubusa.","Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasula dzanja lako kuthambo, kuti pakhale matalala pa dziko lonse la Ejipito, pa anthu ndi pa zoweta, ndi pa zitsamba zonse za kuthengo, m'dziko la Ejipito.","Pamenepo Mose anasamulira ndodo yake kuthambo, ndipo Yehova anatumiza bingu ndi matalala, ndi moto unatsikira pansi; ndipo Yehova anavumbitsa matalala pa dziko la Ejipito.","Potero panali matalala, ndi moto wakutsikatsika pakati pa matalala, choopsa ndithu; panalibe chotere m'dziko lonse la Ejipito chiyambire mtundu wao.","Ndipo matalala anapanda m'dziko lonse la Ejipito zonse za pabwalo, kuyambira anthu kufikira zoweta; ndipo matalala anapanda zitsamba zonse za kuthengo, nathyola mitengo yonse ya kuthengo.","M'dziko la Goseni mokha, mokhala ana a Israele, munalibe matalala.","Ndipo Farao anatumiza, naitana Mose ndi Aroni, nanena nao, Ndachimwa tsopano; Yehova ndiye wolungama, ine ndi anthu anga ndife oipa.","Pembani kwa Yehova; chifukwa akwanira ndithu mabingu a Mulungu ndi matalala; ndipo ndidzakulolani mumuke, osakhalanso.","Ndipo Mose ananena naye, Potuluka m'mudzi ine, ndidzasasatulira manja anga kwa Yehova; mabingu adzaleka, ndi matalala sadzakhalaponso; kuti mudziwe kuti dziko lapansi nla Yehova.","Koma inu ndi anyamata anu ndidziwa kuti simudzayamba kuopa nkhope ya Yehova Mulungu.","Ndipo thonje ndi barele zinayoyoka; pakuti barele lidafula, ndi thonje lidayamba maluwa.","Koma tirigu ndi rai sizinayoyoka popeza amabzala m'mbuyo.","Ndipo Mose anatuluka kwa Farao m'mudzi nasasatulira manja ake kwa Yehova; ndipo mabingu ndi matalala analeka, ndi mvula siinavumbanso padziko.","Pamene Farao anaona kuti mvula ndi matalala ndi mabingu zidaleka anaonjezanso kuchimwa, naumitsa mtima wake, iye ndi anyamata ake.","Potero mtima wa Farao unalimba, ndipo sanalole ana a Israele amuke; monga Yehova adalankhula mwa Mose."]