["Miyambo ya Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israele.","Kudziwa nzeru ndi mwambo;kuzindikira mau ozindikiritsa;","kulandira mwambo wakusamalira machitidwe,chilungamo, chiweruzo ndi zolunjika;","kuchenjeza achibwana,kuphunzitsa mnyamata kudziwa ndi kulingalira;","kuti wanzeru amve, naonjezere kuphunzira;ndi kuti wozindikira afikire kuuphungu;","kuzindikira mwambi ndi tanthauzo lake,mau a anzeru, ndi zophiphiritsa zao.","Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziwa;opusa anyoza nzeru ndi mwambo.","Mwananga, tamva mwambo wa atate wako,ndi kusasiya chilangizo cha amai ako;","pakuti izi ndi korona wa chisomo pamtu pako,ndi mkanda pakhosi pako.","Mwananga, akakukopa ochimwa usalole.","Akanena, Idza nafe, tibisalire mwazi,tilalire osachimwa opanda chifukwa;","tiwameze ali ndi moyo ngati manda,ali amphumphu, ngati akutsikira kudzenje;","tidzapeza chuma chonse cha mtengo wake,tidzadzaza nyumba zathu ndi zofunkha;","udzachita nafe maere,tonse tidzakhala ndi chotengeramo chimodzi.","Mwananga, usayende nao m'njira;letsa phazi lako ku mayendedwe ao;","pakuti mapazi ao athamangira zoipa,afulumira kukhetsa mwazi.","Pakuti kutchera msampha pamaso pa mbalame ndi chabe;","ndipo awa abisalira mwazi waowao, alalira miyoyo yaoyao.","Mayendedwe a yense wopindula chuma monyenga ngotere;chilanda moyo wa eni ake.","Nzeru ifuula panja;imveketsa mau ake pabwalo;","iitana posonkhana anthu polowera pachipata;m'mudzi inena mau ake,","Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu?Onyoza ndi kukonda kunyoza,opusa ndi kuda nzeru?","Tembenukani pamene ndikudzudzulani;taonani, nditsanulira pa inu mzimu wanga,ndikudziwitsani mau anga.","Chifukwa ndaitana, ndipo munakana;ndatambasula dzanja langa,ndipo panalibe analabadira;","koma munapeputsa uphungu wanga wonse,ndi kukana kudzudzula kwanga.","Inetu ndidzachitira chiphwete tsoka lanu,ndidzatonyola pakudza mantha anu;","pakudza mantha anu ngati mphepo yopasula,ndi pofika tsoka lanu ngati kamvulumvulu;pakudza kwa inu vuto ndi nsautso.","Pamenepo adzandiitana,koma sindidzavomera;adzandifunatu, osandipeza ai;","chifukwa anada nzeru,sanafune kuopa Yehova;","anakana uphungu wanga,nanyoza kudzudzula kwanga konse;","momwemo adzadya zipatso za mayendedwe ao,nadzakhuta zolingalira zao.","Pakuti kubwerera m'mbuyo kwa achibwana kudzawapha;ndipo mphwai za opusa zidzawaononga.","Koma wondimvera ine adzakhala osatekeseka,nadzakhala phee osaopa zoipa."]