["Mwana wanzeru amamvera mwambo wa atate;koma wonyoza samvera chidzudzulo.","Munthu adzadya zabwino ndi zipatso za m'kamwa mwake;koma moyo wa achiwembu udzadya chiwawa.","Wogwira pakamwa pake asunga moyo wake;koma woyasamula milomo yake adzaonongeka.","Moyo wa waulesi ukhumba osalandira kanthu;koma moyo wa akhama udzalemera.","Wolungama ada mau onama;koma woipa anyansa, nadzichititsa manyazi.","Chilungamo chitchinjiriza woongoka m'njira;koma udyo ugwetsa wochimwa.","Alipo wodziyesa wolemera, koma alibe kanthu;alipo wodziyesa wosauka, koma ali ndi chuma chambiri.","Chiombolo cha moyo wa munthu ndicho chuma chake;koma wosauka samva chidzudzulo.","Kuunika kwa olungama kukondwa;koma nyali ya oipa idzazima.","Kudzikuza kupikisanitsa;koma omwe anauzidwa uphungu ali ndi nzeru.","Chuma cholandiridwa mokangaza chidzachepa;koma wokundika ndi dzanja adzaona zochuluka.","Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima;koma pakufika chifunirocho ndicho mtengo wa moyo.","Wonyoza mau adziononga yekha;koma woopa malangizo adzalandira mphotho.","Malamulo a wanzeru ndiwo kasupe wa moyo,apatutsa kumisampha ya imfa.","Nzeru yabwino ipatsa chisomo;koma njira ya achiwembu ili makolokoto.","Yense wochenjera amachita mwanzeru;koma wopusa aonetsa utsiru.","Mthenga wolakwa umagwa m'zoipa;koma mtumiki wokhulupirika alamitsa.","Wokana mwambo adzasauka nanyozedwa;koma wolabadira chidzudzulo adzalemekezedwa.","Chifuniro chikondweretsa moyo chitachitidwa;koma kusiya zoipa kunyansa opusa.","Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru:koma mnzao wa opusa adzaphwetekedwa.","Zoipa zilondola ochimwa;koma olungama adzalandira mphotho yabwino.","Wabwino asiyira zidzukulu zake cholowa chabwino;koma wochimwa angosungira wolungama chuma chake.","M'kulima kwa osauka muli zakudya zambiri;koma zinazo zimaonongeka posowa chiweruzo.","Wolekerera mwanake osammenya amuda;koma womkonda amyambize kumlanga.","Wolungama adya nakhutitsa moyo wake;koma mimba ya oipa idzasowa."]