["Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo;koma mau owawitsa aputa msunamo.","Lilime la anzeru linena bwino zomwe adziwa;koma m'kamwa mwa opusa mutsanulira utsiru.","Maso a Yehova ali ponseponse,nayang'anira oipa ndi abwino.","Kuchiza lilime ndiko mtengo wa moyo;koma likakhota liswa moyo.","Chitsiru chipeputsa mwambo wa atate wake;koma wosamalira chidzudzulo amachenjera.","M'nyumba ya wolungama muli katundu wambiri;koma m'phindu la woipa muli vuto.","Milomo ya anzeru iwanditsa nzeru,koma mtima wa opusa suli wolungama.","Nsembe ya oipa inyansa Yehova;koma pemphero la oongoka mtima limkondweretsa.","Njira ya oipa inyansa Yehova;koma akonda wolondola chilungamo.","Wosiya njira adzalangidwa mowawa;wakuda chidzudzulo adzafa.","Kumanda ndi kuchionongeko kuli pamaso pa Yehova;koposa kotani nanga mitima ya ana a anthu?","Wonyoza sakonda kudzudzulidwa,samapita kwa anzeru.","Mtima wokondwa usekeretsa nkhope;koma moyo umasweka ndi zowawa za m'mtima.","Mtima wa wozindikira ufunitsa kudziwa;koma m'kamwa mwa opusa mudya utsiru.","Masiku onse a wosauka ali oipa;koma wokondwera mtima ali ndi phwando losatha.","Zapang'ono, ulikuopa Yehova,zipambana ndi katundu wambiri pokhala phokoso.","Kudya masamba, pali chikondano,kuposa ng'ombe yonenepa pali udani.","Munthu wozaza aputa makani;koma wosakwiya msanga atonthoza makangano.","Mayendedwe a waulesi akunga linga laminga,koma njira ya oongoka mtima iundidwa ngati mseu.","Mwana wanzeru akondweretsa atate wake;koma munthu wopusa apeputsa amake.","Wosowa nzeru akondwera ndi utsiru;koma munthu wozindikira aongola mayendedwe ake.","Zolingalira zizimidwa popanda upo;koma pochuluka aphungu zikhazikika.","Munthu akondwera ndi mayankhidwe a m'kamwa mwake;ndi mau a pa nthawi yake kodi sali abwino?","Anzeru ayesa njira yamoyo yokwerakwera,kuti apatuke kusiya kunsi kwa manda.","Yehova adzapasula nyumba ya wonyada;koma adzalembera mkazi wamasiye malire ake.","Ziwembu zoipa zinyansa Yehova;koma oyera mtima alankhula mau okondweretsa.","Wopindula monyenga avuta nyumba yake;koma wakuda mitulo adzakhala ndi moyo.","Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe;koma m'kamwa mwa ochimwa mutsanulira zoipa.","Yehova atalikira oipa;koma pemphero la olungama alimvera.","Kuunika kwa maso kukondweretsa mtima;ndipo pomveka zabwino mafupa amatenga uwisi.","Khutu lomvera chidzudzulo cha moyolidzakhalabe mwa anzeru.","Wokana mwambo apeputsa moyo wake;koma wosamalira chidzudzulo amatenga nzeru.","Kuopa Yehova ndiko mwambo wanzeru;ndipo chifatso chitsogolera ulemu."]