["Wosauka woyenda mwangwiroaposa wokhetsa milomo ndi wopusa.","Kukhumba kosadziwa sikuli kwabwino;ndipo wofulumira ndi mapazi ake amachimwa.","Utsiru wa munthu ukhotetsa njira yake;mtima wake udandaula pa Yehova.","Chuma chionjezetsa mabwenzi ambiri;koma mnzake wa waumphawi amleka.","Mboni yonama sidzakhala yosalangidwa;wolankhula mabodza sadzapulumuka.","Ambiri adzapembedza waufulu;ndipo yense ndi bwenzi la munthu wopatsa.","Abale onse a wosauka amuda;nanga mabwenzi ake kodi satanimphirana naye?Awatsata ndi mau, koma kuli zii.","Wolandira nzeru akonda moyo wake;wosunga luntha adzapeza zabwino.","Mboni yonama sidzapulumuka chilango;wolankhula mabodza adzaonongeka.","Wopusa sayenera kukhala ndi zinthu zolongosoka;nanga kapolo ayenera kulamulira akalonga kodi?","Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo;ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.","Mkwiyo wa mfumu ukunga kubangula kwa mkango;koma kukoma mtima kwake kunga mame pamsipu.","Mwana wopusa ndiye tsoka la atate wake;ndipo makangano a mkazi ndiwo kudonthadonthabe.","Nyumba ndi chuma ndizo cholowa cha atate;koma mkazi wanzeru achokera kwa Yehova.","Ulesi ugonetsa tulo tofa nato;ndipo moyo wamkhongono udzamva njala.","Wosunga lamulo asunga moyo wake;wonyalanyaza mayendedwe ake adzafa.","Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova;adzambwezera chokoma chakecho.","Menya mwanako, chiyembekezero chilipo,osafunitsa kumuononga.","Munthu waukali alipire mwini;pakuti ukampulumutsa udzateronso.","Tamvera uphungu, nulandire mwambo,kuti ukhale wanzeru pa chimaliziro chako.","Muli zolingalira zambiri m'mtima mwa munthu;koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika.","Chotikondetsa munthu ndicho kukoma mtima kwake;ndipo wosauka apambana munthu wonama.","Kuopa Yehova kupatsa moyo;wokhala nako adzakhala wokhuta;zoipa sizidzamgwera.","Waulesi alonga dzanja lake m'mbale,osalibwezanso kukamwa kwake.","Menya wonyoza, ndipo achibwana adzachenjera;nudzudzule wozindikira adzazindikira nzeru.","Wolanda za atate, ndi wopirikitsa amai,ndiye mwana wochititsa manyazi ndi wogwetsa nkhope.","Ukangofuna, mwananga, kusochera kusiya mau akudziwitsa,leka kumva mwambo.","Mboni yopanda pake inyoza chiweruzo;m'kamwa mwa amphulupulu mumeza zoipa.","Akonzera onyoza chiweruzo,ndi mikwingwirima pamsana pa opusa."]