["Mwananga, usaiwale malamulo anga,mtima wako usunge malangizo anga;","pakuti adzakuonjezera masiku ambiri,ndi zaka za moyo ndi mtendere.","Chifundo ndi choonadi zisakusiye;uzimange pakhosi pako;uzilembe pamtima pako;","motero udzapeza chisomo ndi nzeru yabwino,pamaso pa Mulungu ndi anthu.","Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse,osachirikizika pa luntha lako;","umlemekeze m'njira zako zonse,ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.","Usadziyese wekha wanzeru;opa Yehova, nupatuke pazoipa;","mitsempha yako idzalandirapo moyo,ndi mafupa ako uwisi.","Lemekeza Yehova ndi chuma chako,ndi zinthu zako zonse zoyambirira kucha;","motero nkhokwe zako zidzangoti thee,mbiya zako zidzasefuka vinyo.","Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova,ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake;","pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda;monga atate mwana amene akondwera naye.","Wodala ndi wopeza nzeru,ndi woona luntha;","pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva,phindu lake liposa golide woyengeka.","Mtengo wake uposa ngale;ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye.","Masiku ambiri ali m'dzanja lamanja lake;chuma ndi ulemu m'dzanja lake lamanzere.","Njira zake zili zokondweretsa,mayendedwe ake onse ndiwo mtendere.","Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira;wakuiumirira ngwodala.","Yehova anakhazika dziko ndi nzeru;naika zamwamba ndi luntha.","Zakuya zinang'ambika ndi kudziwa kwake;thambo ligwetsa mame.","Mwananga, zisachokere kumaso ako;sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira;","ndipo mtima wako udzatengapo moyo,ndi khosi lako chisomo.","Pompo udzayenda m'njira yako osaopa,osaphunthwa phazi lako.","Ukagona, sudzachita mantha;udzagona tulo tokondweretsa.","Usaope zoopsa zodzidzimutsa,ngakhale zikadza zopasula oipa;","pakuti Yehova adzalimbitsa mtima wako,nadzasunga phazi lako lingakodwe.","Oyenera kulandira zabwino usawamane;pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino.","Usanene kwa mnzako, Ukabwerenso,ndipo mawa ndidzakupatsa;pokhala uli nako kanthu.","Usapangire mnzako chiwembu;popeza akhala nawe pafupi osatekeseka.","Usakangane ndi munthu chabe,ngati sanakuchitire choipa.","Usachitire nsanje munthu wachiwawa;usasankhe njira yake iliyonse.","Pakuti wamphulupulu anyansa Yehova;koma chinsinsi chake chili ndi oongoka.","Yehova atemberera za m'nyumba ya woipa;koma adalitsa mokhalamo olungama.","Anyozadi akunyoza,koma apatsa akufatsa chisomo.","Anzeru adzalandira ulemu cholowa chao;koma opusa adzakweza manyazi."]