["Ananu, mverani mwambo wa atate,nimutchere makutu mukadziwe luntha;","pakuti ndikuphunzitsani zabwino;musasiye chilangizo changa.","Pakuti ndinali mwana kwa atate wanga,wokondedwa ndi mai, ndine ndekha, sanabale wina.","Atate nandiphunzitsa, nati kwa ine,mtima wako uumirire mau anga;sunga malamulo anga, nukhale ndi moyo.","Tenga nzeru, tenga luntha;usaiwale, usapatuke pa mau a m'kamwa mwanga;","usasiye nzeru, ndipo idzakusunga;uikonde, idzakutchinjiriza.","Nzeru ipambana, tatenga nzeru;m'kutenga kwako konseko utenge luntha.","Uilemekeze, ndipo idzakukweza;idzakutengera ulemu pamene uifungatira.","Idzaika chisada cha chisomo pamtu pako;idzakupatsa korona wokongola.","Tamvera mwananga, nulandire mau anga;ndipo zaka za moyo wako zidzachuluka.","Ndakuphunzitsa m'njira ya nzeru,ndakuyendetsa m'mayendedwe olungama.","Mapazi ako sadzaombana ulikuyenda;ukathamanga, sudzaphunthwa.","Gwira mwambo, osauleka;uusunge; pakuti ndiwo moyo wako.","Usalowe m'mayendedwe ochimwa,usayende m'njira ya oipa.","Pewapo, osapitamo;patukapo, nupitirire.","Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona;ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera.","Pakuti amadya chakudya cha uchimo,namwa vinyo wa chifwamba.","Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha,kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee.","Njira ya oipa ikunga mdima;sadziwa chimene chiwaphunthwitsa.","Mwananga, tamvera mau anga;tcherera makutu ku zonena zanga.","Asachoke kumaso ako;uwasunge m'kati mwa mtima wako.","Pakuti ali moyo kwa omwe awapeza,nalamitsa thupi lao lonse.","Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga;pakuti magwero a moyo atulukamo.","Tasiya m'kamwa mokhota,uike patali milomo yopotoka.","Maso ako ayang'ane m'tsogolo,zikope zako zipenye moongoka.","Sinkasinkha bwino mayendedwe a mapazi ako;njira zako zonse zikonzeke.","Usapatuke kudzanja lamanja kapena kulamanzere;suntha phazi lako kusiya zoipa."]