["Mwananga, mvera nzeru yanga;tcherera makutu ku luntha langa;","ukasunge zolingalira,milomo yako ilabadire zomwe udziwa.","Pakuti milomo ya mkazi wachiwerewere ikukha uchi;m'kamwa mwake muti see koposa mafuta.","Chimaliziro chake nchowawa ngati chivumulo,ndi chakuthwa ngati lupanga lakuthawa konsekonse.","Mayendedwe ake atsikira kuimfa;mapazi ake aumirira kumanda;","sasinkhasinkha bwino za njira ya moyo;mayendedwe ake adzandira dzandidzandi osadziwa iye.","Ndipo tsopano ana, mundimvere,musapatuke ku mau a m'kamwa mwanga.","Siyanitsa njira yako kutali kwa iyeyo,osayandikira ku khomo la nyumba yake;","kuti ungapereke ulemu wako kwa ena,ndi zaka zako kwa ankhanza;","kuti mphamvu yako isakhutitse alendo,ndi kuti usagwire ntchito m'nyumba ya wachilendo;","ungalire pa chimaliziro chako,pothera nyama yako ndi thupi lako;","ndi kuti, Bwanji ndinada mwambo,mtima wanga ndi kunyoza chidzudzulo;","ndipo sindinamvera mau a aphunzitsi anga;ngakhale kutcherera makutu kwa akundilanga mwambo!","Ndikadakhala m'zoipa zonse,m'kati mwa msonkhano ndi khamu la anthu.","Imwa madzi a m'chitsime mwako,ndi madzi oyenda a m'kasupe mwako.","Kodi magwero ako ayenera kumwazika kunja,ndi mitsinje ya madzi m'makwalala?","Ikhale ya iwe wekha,si ya alendo okhala nawe ai.","Adalitsike kasupe wako;ukondwere ndi mkazi wokula nayo.","Ngati mbawala yokonda ndi chinkhoma chachisomo,maere ake akukwanire nthawi zonse;ukodwe ndi chikondi chake osaleka.","Pakuti ukondwerenji, mwananga, ndi mkazi wachiwerewere,ndi kufungatira chifuwa cha mkazi wachilendo?","Pakuti njira za munthu zili pamaso pa Yehova,asinkhasinkha za mayendedwe ake onse.","Zoipa zakezake zidzagwira woipa;adzamangidwa ndi zingwe za uchimo wake.","Adzafa posowa mwambo;adzasochera popusa kwambiri."]